THE HISTORY OF SOCCER IN MALAWI.

COMPUTURER REPAIRS AND PHONE

THE HISTORY OF SOCCER IN MALAWI.

tnm_12_02

At Likoma the Anglicans were also more into football. By 1910 the Anglicans at Likoma came with a book of rules standardising the game of football for the first time in Nyasaland.
They believed that in football native students would embrace the virtues of English self discipline and fair play.
The Blantyre mission built the first football pitch in Nyasaland at HHI still surviving to date. .. which was later to be used by Michiru Castles, one of the oldest clubs in Nyasaland.
In 1920s other bodies – the Police formed in 1923, Prison, Boma administrative staff formed teams which took part in football matches.
The foundation of Ndirande Welfare Club in 1933 by the Likes of Sangala, Lawrence Makata and Lali Lubani ensured that football was organised on a formal basis.
Ndirande Welfare Club which controlled football issues inter alia was run by a group of mission educated clerks and businessmen. The club had its own football pitch where it played regular matches against Jeanes College FC of Domasi.
The oldest and first company sponsored team in Nyasaland was Nyasaland Railways FC.
In 1937 Levi Mumba convined a meeting in Lilongwe stating that immediate steps were to be taken to revive sports in Nyasaland particularly football.
Observations at the meeting were that football was not being played regularly in Nyasaland due to lack of ‘ball or ground.’
Former soldiers of KAR, workers returning from Salisbury and South Africa became very involved in football.
The key development in Nyasaland football was in 1938 with the formation of the Shire Highlands African League.
In 1939, the Nyasaland Railways began to run the ‘football specials’ between Blantyre and Limbe taking fans to some of the matches using company transport.
Nyasaland interest in football grew so tremendously that in 1946, teams from Chileka and Lunzu were incorporated into the Shire Highlands League including Michiru Castles of Chilomoni.
That year the climax was the Nyasaland Amateur Football Cup final between Abraham FC of Blantyre vs Zomba Amateur Athletic FC.
In a rare outbreak of multiracialism the game was played at Blantyre Sports Club.
The game attracted a large crowd across racial barriers. ..Indians, Europeans and the natives.
Abraham FC of Blantyre won the cup 2-1.
James Sangala one of the founders of Nyasaland African Congress was the Chief Organiser of the League.
Sangala was also the manager of Shire Highlands Select which played Grupo Desportivo Rebenta Fogo of Beira in 1949.
This was the first international match that Nyasaland played.
By this time, Nyasaland Football Association had been formed with teams like Imperial Tobacco Co FC taking on existing favourites Michiru Castles of Chilomoni, Abrahams FC and Ndirande Lions.
In 1962 Nyasaland played Westham FC of London in Blantyre at Rangeley Stadium and later played Ghana the African Champions and lost 12-0 with the likes of Nyasaland prolific striker Godfrey Kalitsiro, Roy Maliwa, Raleigh Mmanga, Richard Banda, Oliver Nankhumwa, Lee Mlanga in the team
Nevertheless in June 1964 Nyasaland played against Southern Rhodesia at Rangeley in Blantyre and drew in presence of 50, 000 spectators.
In July 1964 the Mufulu Cup was the first cup organised by an independent African state in Southern Africa.
Nyasaland organised this cup which involved Northern Rhodesia,Nyasaland and Tanganyika.
The development of football in Nyasaland was done by different dedicated men who knew when to go after their contributions
In 1968, Sidney Chikafa one of the old players in Nyasaland formed the Football Association of Malawi and became it’s first President.

THE MEANING OF KALINDO.

COMPUTURER REPAIRS AND PHONE
tnm_12_02

CADET EYES
THE MEANING OF KALINDO.
Kalindo is a yao word and it simply means small shelter.
If its big or bigger is called chilindo.
These kalindos are built at your farm yard. You put your things there while you are busy kulima. You put things like water or thobwa and other stuff. When it is raining you run to kalindo or chilindo and hide yourself there. So for some of you who don’t know yao please take note.
Don’t rely on Kalindo, it’s just a shelter, something like bus shelter, when the bus comes all the people will rush to the bus leaving kalindo alone, No occupants. If you hear someone saying that am kalindo just know that its a small temporary shelter. It can take only few people and those few people very soon, will leave it alone because its just kalindo, a small shelter.

Star of to day /mbili _BINGU WA MUTHALIKA .

COMPUTURER REPAIRS AND PHONE

BINGU WA MUTHALIKA
.
Ryson

tnm_12_02

webster thom amene anasitha dzina 1960 kukhala bingu wa mutharika.
anabadwa
pa
24 february, 1934.
ku
thyolo
ndipo
bambo ake a ryson mutharika anali mphunzitsi
komanso
mai ake anali mkuru wa amayi amvano ku ccap.
Sukulu yake ya ku pulayimale anaphunzira ku ulongwe mission,
ku chingoli,
ku mtambanyama,
ku malamulo
kenaka
ku henry henderson institute ku kabula [blantyre]. kenaka bingu, sekondale anakaphunzira ku dedza secondary school
komwe anatenga CAMBRIDGE OVERSEAS SCHOOL LEAVING CERTIFICATE ndi grade A mu 1965.
Bingu anali nawo mundanda wa anthu amene anasankhidwa
ndi
malemu ngwazi dr hastings kamuzu banda, kukaphunzira maphunziro aukachenjede ku india.
ku india, bingu anatenga BANCHELOR DEGREE IN ECONOMICS pa shri ram college of commerce
komanso
M.A DEGREE IN ECONOMICS
ku
delhi school of economics.
Mutharika adatenga PHD DEGREE ku pacific western university.
kuphatikiza apa, bingu anapanga timaphunzira tina tokhuzana ndi business management,
financial analysis,
trade promotion,
political leadership,
regional economic co-operation and human relation.
bingu wagwirapo ntchito. ma boma a malawi ndi zambia
ngati
administrative officer
komanso
anapasidwa mwayi okhala deputy governor wa RESERVE BANK OF MALAWI.
Mu chaka cha 2002, bingu adasankhidwa kukhala nduna ya zachuma ndi ma plan a chitukuko.
Kupatura kugwira ntchito boma, bingu wagwirapo ntchito ku WORLD BANK ngati loan officer,
wagwiranso ku UN economic commision of africa ngati director of trade and development finance.
komanso
wagwirapo ngati General secretary ku bungwe la COMESA.
bingu ndale anayamba 1998
ndipo
anayima nawo pachisankho cha 1999 , ndi chipani chake cha united party.
ndipo pachisankhocho , bingu ndi united party, anamaliza ngati chitsekera khomo
kenaka
mu chaka cha 2004, anasankhidwa ndi dr bakiri “a chair” muluzi
ngati
mlowa malo wao komanso ozayimira chipani cha united democratic front[UDF] pachisankho cha 2004.
chomwe anawina koma kenaka anatuluka mu udf ndipo anakayambitsa chipani chake cha dpp.
Anatuluka mu Udf, kamba koti mu udf, dr muluzi ankafuna azimuuza zochita ndipo iye anangochokamo.
mu term yoyamba ya bingu zinthu zinali bwino kwambiri.
pa nkhani ya chuma ndi ulimi.
kamba koti athu ankalandira makuponi omwe amawapangitsa kugura zipangizo za ulimi motsika mtengo zomwe zinapindulira amalawi ovutika ndi osauka okwana 1.7million.
ndipo
zotsatira zake anthu amakolora zolima zambiri.
mpaka mu zaka za 2005/2006, malawi inali ndi chakudya chokwana 500000 metric tones.
Komanso
mu zaka za 2008/2009, malawi inali ndi chimanga chokwana 1.3 milion metric tons ndipo ichi chinali chakudya chokwanira kudya chaka chonse.
mpakana china kugulitsanso ndipo izi zinapangitsa anthu kumutcha ngwazi kamba koti ulamuliro wake umafanana ndi wa malemu dr. Hastings kamuzu banda, omwe amalimbikitsa ulimi. komanso izi zinapangitsa oyimba otchedwa joseph nkasa kuimba nyimbo yomwe bingu ankamufanizira ndi mose wa ku israel……..
.

Bingu anawinanso, pachisankho cha 2009.
Bingu mu ulamuliro wake kuchokera 2004-2009,
anakwanitsa zinthu ngati izi,
malawi inali ndi chakudya chokwanira
komanso
chuma chimayenda bwino. kamba koti amakana kugwetsa mphamvu ndalama ya kwacha
malingana ndi momwe amafunira maiko ena, omwe amathandiza malawi.
komanso
bingu, amalimbikitsa chitukuko cha kumidzi
ndi
zina zambiri, kamba ka ndondomeko yomwe iye anayambitsa yogawa makuponi,
anthu anali ndi chakudya chambiri
ndipo
umphawi unachepa kuchoka pa 52% kufika pa 40%
komanso
dziko la malawi inakwera pandanda wa maiko osauka zomwe zinapangitsa iye kusankhidwa kukhala mkuru wa African Union
ndipo kenaka
iye
anayambitsa ndondomeko yomwe amaitcha ” african food basket “.
komanso
anapempha mtsogoler i wa ku ivory coast, laurent gbagbo,
kuti atule pansi udindo, pamene adaluza zisankho.
Bingu anakhala nawo pa mwambo olonga,
paul kagame kukhala pulezidenti ku Rwanda.
Pamene malawi inkapangitsa mkumano wa AU,
khothi lalikuru padziko lonse la International Criminal Court[ICC],
linapempha dziko la malawi. kuti agwire pulezidenti wa ku sudan, omar al bashil.
koma
bingu anakana.
Bingu anapangitsa zoti, Pa budget ya chaka chonse pazikhala 11%
yomwe
imapita ku makuponi. bingu anawina pa chisankho cha 2009.
pamodzi
ndi
ng’ono wake, prof.arthur peter mutharika, amene anayimira uphungu
ku
thyolo
komanso
ndi wachiwiri wake joyce banda amene anamuchotsa mu chipani cha dpp kamba kotsutsana ndi maganizo okuti peter azayimile pa zisankho za 2014
malo mwa iye, joyce banda.
Malemu ngwazi,
bingu wa mutharika, anathamangitsa kazembe wa ku britain kuno ku malawi, mr cochrane dyet.
kamba ka mau ake okuti bingu samamva zamunthu.
komanso
samapepeseka.
ndipo kenaka, nayonso britain inathamangitsa kazembe wa ku malawi ku britain, mr. chidyaonga. komanso inasiya kuthandiza dziko la malawi.
kenaka
bingu anapepesa ku britain
koma
britain sinatumizenso kazembe ku malawi kufikira kumwalira kwake.
Bingu ndi amene anasitha mbendera
kuti
ikhale yadzuwa ikuwala yonse [kutanthauza kuti malawi ndi dziko tsopano yoyimadi payokha].
koma kena a joyce banda anaibwezeletsanso mbendera ija kukhala yakale pomwe iwo adalowa boma.
Pamene zinthu zinayamba kuvuta,
kamba
kakukwera mtengo kwa zinthu. ndikusowa kwa mafuta oyendera, anthu anapanga zionetsero zomwe zinapha anthu 20. ndipo iye bingu, anati athana ndi aliyense otsutsa ” i will continue smoke out my enemies”.
Zinthu zina zomwe a malawi amaziyamikira zomwe anapanga
komanso
ankafuna kupanga bingu,
ndi miseu,
5 star hotel,
new parliament,
doko la nsanje
ndi
bwalo la zamasewero lomwe lili Ku Lilongwe [BNS
komanso
MALAWI UNIVERSITY OF SCIENCE,
UNIV OF COTTON RESEARCH,
UNIV OF MARINE BIOLOGY, izi ndi zina za mu chitukuko cha malemu bingu.
Bingu anali wa katolika ndipo mkazi wake oyamba, ethel zvauya anamwalira
pa
28 may, 2007.
ndipo
anabereka naye ana anayi,
duwa
tapiwa
noma
madalitso.
kenaka
bingu, anakwatira callista mu chaka cha 2010.
Bingu anamwalira pa 5 april, 2012. koma zinatsimikizika
pa 7 april, 2012. pamene anapita naye kuchipatala cha ku south africa ndipo anamwalira ndi nthenda ya cardiac arrest or heart attack [iyi ndi nthenda imene, mtima umasiya kapena kulephera kupopa magazi].
Bingu ng’ono wake, peter mutharika ndi lecture wakale kale
wa
washington university.
ndipo
pakali pano,
prof. Arthur peter mutharika
ndi
pulezidenti kuno kumalawi.
Bingu ndi amene anayambitsa buget ya zero-budget, yomwe simadalira ndalama za kunja.
komanso bingu, anali mwini wa bingu silvergrey foundation, yomwe imathandiza okalamba,
aumphawi
ndi
amasiye.
Bingu anali sponsor wa tigrisses netball club.
Awa ndi Ma awards, omwe bingu adalandira.
-milenium development goal award, kamba kothetsa njala
-comesa distinguished award
– medal glory award kamba koyendetsa bwino chuma
-the most excellent grand commander award
-danish gat award kamba kotukula azimayi.
Mau amalemu prof. Bingu wa mutharika ” dziko la malawi silosauka koma anthu okhala dzikomo ndiye osauka”.
Bingu adapatsidwa dzina la ” kasupe wanjanji ndi amalawi”.
Malingana ndi t.b.joshua, zidaonetsa kuti bingu adalemberedwa kalata ndi prophet t.b.joshua, zomuuza za imfa yake
ndipo
adavomera kuti zikhale mene mbuye wakonzera.
Bingu asadamwalire, T.b.joshua adali atalosera kale kuti ku kumwera kwa africa, pulezidenti amwalira.
.
[REST IN PEACE]
.

star walero /mbili-EVISON MATAFALE

Matafale-640x960

COMPUTURER REPAIRS AND PHONE
tnm_12_02

EVISON MATAFALE
.
Hee kaya e-kayeeee!
Waseselekaaa!
…………………………………………..
Eyayaa…..E-yaaaaaa!!!
Kodi tidanilananji?
Yang’ana nkhope yako, yang’ana nkhope yanga, zimangofanana…
Tifanana ndi Mlengi.
.
EVISON MATAFALE anabadwa mu chaka cha 1969 mudzi mwa a Singano ku Chileka boma la Blantyre.
Matafale anakula ali membala wa Seventhday Aventist Church ndipo kenako atasinkhuka msinkhu anayamba kusatila chikhalidwe cha chi Rasta.
.
Malingana ndi mpingo wa ma Rasta muno Malawi, Evison Matafale akuti anali Prophet kapena kuti neneli ozozedwa ndi Mulungu (Jah Rasta Farrai) wa mpingowu kuno ku Malawi.
Matafale analiso ndi luso loziwa kupeka nyimbo komanso kaswiri oyimba nyimbo kuno ku Malawi mu chamba chija Reggae.
Iye anapasidwa udindo kuti ndi mfumu ya reggae muno Malawi.
.
MOYO WAO MU MUSIC
…………………………………………
Evison Matafale anayamba kuyimba ali wachichepele ndipo anali membala wa choir ku church cha Seventhday.
Kenako iwo atakula anajowina gulu lina loyimba lotchedwa Welling Brothers komwe iwo mu 1999 anatulusa chimbale chao choyamba chotchedwa kuyimba 1 momwe munali nyimbo yomwe inatchuka kwambiri; ”Waseseleka”.
Kenako mu chaka cha 2000 iwo anatulusa chimbale china chotchedwa ‘kuyimba 2’ ndipo menemo kuti atayambisa gulu lawo lotchedwa BLACK MISSIONARIES ndipo mu chimbale cha kuyimba 2 munali nyimbo zambiri zomwe zintchuka kwambiri.
Nyimbo za Matafale zinakondedwa ndi anthu ambiri ndipo mkuluyu anatchuka kwambiri.
.
Evison Matafale nyimbo zake zinali zozuzula komanso kufalisa uthenga ndi kuyanjanisa mitundu monga momwe mpingo wa ma Rasta umalimbikisila ma membala ake kuti azikhala patsogolo pobwelesa mtendere pakati pa anthu onse a mitundu yosiyana.
Matafale analiso munthu osapsatila mau akafuna kuyankhula ndipo anaziwika pakati pa abale ake komanso pakati pa azizake kuti iye anali munthu osabisa chichewa akafuna kuyankhula.
Ngati zinthu zakhota kapena kupindika, iye anali kuzuzula pomwepo.
.
Ku mayambiliro a chaka cha 2001, Matafale anadwala nthenda ya TB (tuberculosis) ndipo izi zinapangisa kuti iye achose sisi lake lomwe linali lalitali-litali mutu mwake (dreadlocks).
Pa nthawi imeneyi, kunali ziii ndipo mkuluyu anasowa kwambiri ndipo mphekesela chabe ena ankanena zoti mkuluyu ali ku America pomwe ena ankati mkuluyu anayamba ntchito ya uphunzisi.
.
Mu September 2001, Matafale anajambula nyimbo yotchedwa ‘Time mark” nyimbo yomwe anayimba patangochitika chiwembu chomwe gulu la Al Qaeda linaphulisa ndi mabomba ku Washingtone dziko la America.
Kenako Matafale analemba kalata kulembela tsogoleri wa dziko pa nthawiyo a Bakili Muluzi ndipo mukalatayo anazuzula utsogoleri wa a Muluzi kuti unali okondela a silamu komanso amwenye omwe amachita malonda dziko muno.
.
Matafale anapitiliza kuzuzula utsogoleri wa nthawiyo, utsogoleri wa Bakili Muluzi.
Matafale anapita ku shop ya mwenye wina komwe anakapangako chipwilikiti ndipo iye pa 24 November, 2001 anamangidwa ndi a polisi.
Mene amamangidwa, kuti iyeyo akuvutika ndi Malungo ndipo mayi ake anayesela kuwadandaulira apolisi kuti mwana wawoyo akudwala koma apolisi anawalimbisa mtima mayiwo kuti mwana wao akungofuna akafunsidwe mafunso ku polisi ndikuti posachedwa abwelera naye.
Pakati pa usiku, Matafale ananyamulidwa ndi a polisi kupita naye ku Lilongwe ndipo malingana ndi chimwene wake wa malemu Matafale ‘Elton’, Matafale akuti anazuzidwa kwambiri, kumenyedwa, komanso anamuponya mu galimoto la polisi atamumga unyolo koma osamuveka malaya.
.
Sipanapite nthawi, Matafale anamwalira kundende.
Thupi lake litayezedwa, bambo Charles Mwansambo anatulusa lipoti loti Matafale anafa ndi nthenda ya chibayo.
Nalo lipoti lochokela ku polisi limanena zoti Matafale anafa chifukwa cha nthenda osati chifukwa chozuzidwa kapena kumenyedwa.
.
Ifa ya Matafale, inabwelesa nkhani zambiri pakati pa a Malawi ndipo anthu ambiri amazuzula utsogoleri wa nthawiyo kuti unatengapo gawo pa ifa ya malemuwa.
Ku mwambo wa maliro omwe unachitikila ku Chileka, kunapita anthu ambiri ndipo mwambowu unayendesedwa ndi azathu a mpingo wa chi Rasta.
Malemuwa anasiya mwana modzi yemwe ndi tsikana.
.
Matafale analosela za ifa yake pomwe anayankhula mau oti;
”sindiopa munthu yemwe amapha thupi chifukwa baibulo likundiuza kuti ndikuyenela kuopa yemwe angathe kupha thuphi ndi mzimu omwe”
.
Band yomwe anayambisa Matafale idakalipo ndipo ikupitililabe kutisangalasa ndi nyimbo zawo muno Malawi.
.
Pa 6 July, 2010 tsogoleri wa dziko lino pa nthawiyo malemu Professor Bingu wa Munthalika anapeleka award kwa malemu Evison Matafale ngati modzi mwa a Malawi omwe anapanga zinthu zolozeka ku dziko la Malawi ndipo a kubanja la malemu Matafale ndiye anatenga award imeneyi komanso mphatso ya ndalama inapelekedwa ku banjali.
.
Matafale anapita, koma nyimbo zake ndi uthenga omwe anayika mu nyimbo zakezo ulipo mpaka lero.
Olakwa ndani?

Star of today ,mbili ➡SOLDIER LUCIUS BANDA

COMPUTURER REPAIRS AND PHONE
tnm_12_02

SOLDIER LUCIUS BANDA
.
Lucius Banda anabadwa pa 17 August chaka cha 1970 mudzi mwa Sosola, Group Village headman Kapalamula, mfumu yaikulu Nsamala ku Balaka.
Anaphunzira maphunziro ake a ku Primary pa sukulu ya Mponda yomwe ili pafupi ndi Parish ya Balaka.
Lucius Banda Maphunziro ake sadathele ku Primary, anapitiliza mpaka ku Secondary school.
.
MOYO WAKE MU MUSIC
………………………………………….
LUCIUS Banda anayamba kuyimba chaka cha 1983 menemo kuti ali ndi zaka 13 ndipo adali ali ku primary school.
Ndipo yemwe anali kumuthandizila pa mayimbidwe ake anali chimwene wake Paul Banda yemwe ndi tsogoleri komanso yemwe anayambisa gulu la Alleluya Band.
Lucius Banda anayimba pa stage koyamba pamaso pagulu mu chaka cha 1985 ndipo panthawiyo anali nawo mugulu la Alleluya Band mosogozedwa ndi Paul Banda.
.
Malingaliro ofuna kutukula luso lake anamuzela ndipo anaganizila zopita ku South Africa kuti akaphunzile mayimbidwe ndikupitisa patsogolo luso lake.
Maloto ake anakwanilisidwa pomwe mu chaka cha 1993 anajowina gulu lina la ku Johannesburg Lotchedwa DORKEY HOUSE ndipo kumeneku anakhalako chaka chimodzi.
Anajambula Album yake yoyamba yotchedwa “SON OF A POOR MAN” ndipo anajambulira ku Standel Music Studio, producer wake anali George Arigone wa ku Argetina. Ndipo omwe anamuthandizila ma backing vocals anali Nomahalanla Nkhize komanso oyimba wina wa nyimbo za uzimu Debora Freser.
Album imeneyi munali nyimbo ngati ”MABALA, GET UP STAND UP, LINDA, AND LIFE ON EARTH”.
Nyimbo ya Mabala inatchuka kwambiri. Nyimboyi inali yandale yomwe imafotokoza za nkhaza zomwe zinalipo mu ulamuliro wa Malawi Congress Party. Nyimboyi inali ndi mawu oti;
”kukhululuka ndiye takhululuka, koma mabala ndiye akupweteka…..
Kenako amazati;
”tavesela iwe zanga olira, nkhuku ija yafa, mdima wathawa ndipo nyali yawala..”
Ndipo chorus yake amazati;
”inu mumati zizakhala chochi, mpaka liti abale? Ana a Mulungu sangakhalire kulira masiku onse a moyo wao”…
Kuyivesela bwino nyimboyi, inali yolira komanso linali pemphero.
.
1994, Malawi Congress Party inachoka m’boma ndipo ufulu wa mayimbidwe unapelekedwa.
Mongokukumbusani, Nthawi ya Malawi Congress Party samalora munthu kuyimba nyimbo mwachiswawa. Munthu ukajambula nyimbo yako, imayenela iveseledwe kaye ndi akulu akulu a boma ndipo kenako akupase chilolezo kapena nyimbo yakoyo amayikana kuti siyololedwa kuyimbidwa muno Malawi.
Nthawi inayake oyimba winawake wa ku America anayimba nyimbo yotchedwa ”Ceicilia please come back, I’m down on my knees”
nyimbo imeneyi inangolira kamodzi pa MBC koma yemwe anayisewela pa Radio pa nthawiyo ntchito inawuma ndipo nyimboyi inalesedwa kuti isazavekeso chifukwa munyimboyi munali dzina la Mama wa fuko la Malawi.
Koma 1994, ufulu unapelekedwa ndipo oyimba anayamba kuyimba nyimbo mwa ufulu.
.
1997, Lucius Banda anatulusa album yake ya nambala 4 ndipo imeneyi mutu wake unali ”Yahwe”.
Mu album imeneyi munali nyimbo monga; ”Njoka mu Udzu” nyimbo yomwe imadzuzula mabwana ma office. Munaliso nyimbo monga; ”MUKAWAUZE” yomwe imakumbusa anthu za nkhaza za Malawi Congress Party. Nyimbo ya ”Mukawauze” chorus yake imaveka chochi;
….mukawauze anawo asatengeke, njoka ndi njoka singasinthe manga………
Ndipo album yomweyi ya Yahwe munaliso nyimbo yomwe anayimbila malemu mayi ake yomwe imati; ”chabwino mayi zembani, mupume mu mtendere, kumwamba muli amayi mukoze malo anga….
Ndipo kenako chaka chomwechi Lucius Banda anakhazikisa gulu lake loyimba lotchedwa Zembani Band.
.
Gulu la Lucius la Zembani Banda linatulusa oyimba ambiri omwe nthawi inayake anatchuka kwambiri monga; Billy Kaunda, Enort Mbandambanda, Mlaka Maliro, Charles Nsaku, Pat Abig Tung’ande, Emma Masauko, Wendy Harawa ndi ena ambiri kuphatikizapo Lameck Katunga komanso Dan-Lu.
.
Lucius Banda ndi oyimba oyamba wa kuno ku Malawi kuyimba nyimbo zozuzula Ngwazi Kamuzu Banda mu nthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi.
.
MOYO WANDALE
……………………………….
Lucius Banda ndi phungu wa kunyumba ya Malamulo wa chipani cha UDF.
Kanthawi kenakake, Lucius Banda analamulidwa ndi court kuti sali ololedwa kukhala phungu wa kunyumba ya malamulo chifukwa choti analibe mapepala a form 4.
Lucius Banda mu 2005 pomwe malemu Bingu ndi Muluzi ubale wao sunali bwino, iye anayimba nyimbo yoti ”njobvu zikamamenyana umavutika ndi udzu chonde tagwilizanani”
inali nyimbo yabwino kwambiri chifukwa munali uthenga wa mtendere zomwe zinasonyeza kuti mkuluyu ndi wa mtendere.
.
Nthawi inayake anadana ndi Bingu ndipo anayamba kuyimba nyimbo zonyoza Bingu, mpakana anamangidwa. Koma atamwalira Bingu, Lucius analiuza dziko kuzela mu nyimbo yake kuti Bingu anali mamuna olikonda dziko.
.
Lucius Banda adakayimbabe ndipo ndi Legend wathu pa mayimbidwe.