MUTU WACHING’ALANG’ALA (MIGRAINE HEADACHE)

COMPUTURER REPAIRS AND PHONE

HEALTHY/ZAUMOYO
MUTU WACHING’ALANG’ALA (MIGRAINE HEADACHE)
Anthu ambiri tikadwala mutu umangokhala chizindikiro cha matenda ena mwachitsanzo malungo,chifuwa/chimfine kapenanso tikakhala ndi infection penapake mthupi.
Enanso timadwala mutu tikagwira ntchito yolemetsa kapena kukhala ndi nkhawa.
Mitundu ya kuwawa kwa mutu kumeneku sikumadetsa nkhawa kweni kweni chifukwa munthu akachira malungo,chimfine kapena matenda ena mutu umasiya.Munthunso akamwa ma painkiller mutuwo umazizira.
Komano pali mtundu wa mutu uwu timati migraine headache.Kuwawa kwa mutu kumeneku kumasowetsa mtendere anthu ena moti ukayamba sangagwire ntchito. Mutuwu nthawi zambiri umawawira mbali imodzi ndipo kuwawa kwake umamveka mobaya chamkatikati.
Mutu waching’alang’ala umatha kumuvutitsa munthu kwa ma minutes ochepa koma ena mpaka kwa masiku atatu akuvutikabe kenako amapeza mtendere.
Ena amaumvera kuwawira mmaso ndipo amatha kuona mdima ndi chizungulire,kufuna kusanza kapena kusanza kumene,kufooka komanso mutu kupepuka.
Mutuwu umatha kumaonjezereka akaona kuwala,kumva phokoso,ngati asagone mokwanira komanso akakhala ndi nkhawa.
Migraine imakonda kugwira azimayi kuposa abambo ndipo nthawi zina munthu umatha kuzitengera ku makolo.
Chomwe chimayambisa Mutuwu sichidziwika koma timakhulupilira kuti misempha ya muuobongo ndi imene zimapangisa.Pamene misempha ina yatupa chifukwa chakusokonekera kwa michere ina izi zimapangisa kuwawa kumeneku.Nthawi zina amzathu achizimayi umatha kuwayamba akayamba nsambo wa pa mwezi chifukwa cha kusintha kwa michere ina mthupi mwawo (ma hormones)

NDINGATANI NGATI MUTUWU UKANDIVUTA
Ndibwino kuonetsetsa kuti mwapewa zomwe zimapangisa kuti mutu ukuyambeni monga kukhala padzuwa nthawi yaitali,kusagona mokwanira kapena kugona moonjeza,kukhala pa phokoso,kudumphisa ma meals ena,Kumwa coffee moonjeza ndi zina.
Pumulani mokwanira mutuwu ukayamba komanso mutha kukhala mu room yomwe mulibe light.

tnm_12_02

Mutha kumwanso ma painkillers monga panado,brufen ndi ena monga betapayne or syndol kuti kuwawa kuchepe.Musamwe ma pain killer moonjeza chifukwa amathanso kukoledzera mutuwu.Ngati kuwawa sikukusintha kwa masiku ambiri pitani kuchipatala mitundu ina ya mankhwala ilipo kuti mupeze bwino.

Leave a comment

Leave a Reply

Be the first to comment on "MUTU WACHING’ALANG’ALA (MIGRAINE HEADACHE)"

Leave a comment

Your email address will not be published.


*


");pageTracker._trackPageview();
%d bloggers like this: