Mubanja lina lopemphera munabuka phokoso

COMPUTURER REPAIRS AND PHONE

Mubanja lina lopemphera munabuka phokoso kaamba koti Mkaz wa m’banjali ankaganizira kuti mwamuna wake akumuyenda njomba, inde ali ndichibwènzi.

Izitu zinali choncho kaamba kakuti utsiku wina akugona pa fon ya amuna awo panabwera text yooneka yachikondi kuchokera kunambala yomwe imaoneka kuti inali yachilendo.
Mwanuna anayesesa kukana kuti sakudziwapo kanthu koma mkaz anakanika kumvetsa kumati mwamunayo ndi HULE chàbe amangobisala mukupemphera.

Zinatenga ndithu matsiku nyumba mukungokhala ngt ku WARD YA ANA liliphokoso…mkaz atalutsa kwambiri ndipo anati sakwanitsa kukhala ndi mwamuna wachimasomasoyo.
Mwamunayu analidi opemphera ndipo anachiikiza ichi m’manja mwa Ambuye koma sizinasinthe kukangana kuja, kufikira mkaz anamuuza kut amanga zake azipita.

Mwamuna anayesa kulilira kwa Mulungu kuti akuloleranji kuti nyengo izi zimufikire, koma kunena zoona panalibe yankho looneka kwa bamboyu, angakhale anali ndi umboni kuti Mulungu amayankha.
Tsiku limenelo chakumasana bambo uja anaona nkaz wake akupakila zinthu zake expand kut basi akupita.
Nayeso mwamuna ataona kuti zavuta, nayenso anangoyamba kupakira bag yake kuti nayenso azipita kwao.

Mkaz uja anali odabwa ndizomwe amachita mwamuna wakeyo…
“KODI SOPANO NDIYE INU MUKUPITA KUTI?
anafunsa mkaz modabwa ndipo mwamuna uja anati;
“INENSO NDIKUPITA KWA MAI ANGA..”
Mkaz anachita kuziimika bwino kuti amvetsetse, ndipo anati;
“TSONO NANGA ANAWA”?

Mwamuna anangomwetulira kenako anati;
“INU MUKUPITA KWA MAI ANU, INENSO NKUPITA KWA MAI ANGA, IWONSO APITA KWA MAI AWO”..
Mkaz anagwa nalo phwete ndipo anabwera nkumukumbatila mwamuna wake nkumuuza kuti amamukonda zonse zatha…
Mtendere unabwereranso ndipo anayamba kukhala bwino ngat kale…
Utsiku wina alikugona mkaz uja anamufunsa mwamuna wake;
“BAMBO AYANKHO, KODI NZERU IMENE IJA MUNAIGANIZA BWANJI YOTI NANUNSO MUPAKILE BAG YANU;
Komatu munthawi iyi mwamuna uja anali ali mumisoz kulira ndithu ndipo anati;
“KUTERO NANENSO NZOMWE NKUGANIZIRA APAPA KUTI NDINAGANIZA BWANJI ZIMENE ZIJA, NDINAYESA KUKUNYENGERERA UNAKANIKA, KOMA PANO NDIKUTHA KUONA KUTI ANALI MULUNGU YEMWE ANANDIPATSA NZERU IJA, POYAMBA NDINKAONA NGAT MULUNGU SANANDIYANKHE, KOMA PANO NDIKUONA KUTI CHIGANIZO CHIJA SINALI NZERU YANGA YOKHA KOMA KUCHOKERA KWA MULUNGU KUDZERA MWA MZIMU OYERA.”
Onse anachita mantha ndipo anapatsa Mulungu ulemu ndikumutamanda.

Mulungu ali nazo njira zambiri zomwe amayankhila maka iwe wekha ukamukhulupira mkat mwako kuti uyankhidwa…amatha kuyankha osati momwe iwe mwini unali kuyembekezera koma amakhala kuti wayankha basi…
MACHITIDWE 1 VS 8, Imakamba za mzimu OYERA amene Ambuye analonjeza momwe nakpita kumwamba kuti azizakhala ndiife nthawi zonse. MACHITIDWE 2 VS 4, Imatitsimikizira zakulandilidwa kwa MZIMU OYERA…akuti NDIPO ONSE ANADZADZIDWA NDI MZIMU OYERA.
Kutero panopa aliyense akuyenera kukhala ndi MZIMU oyera…kutero yemwe anapangitsa bambo uja kupanga choganizo chobweletsa ntendere m’banja lake ndi MZIMU OYERA amene amakhala mwaiye.
Aliyense ali nawo MZIMU OYERA koma mwaena sakugwira ntchito monga zimayenera kukhalira.. MZIMU OYERA samakhala active(kugwira ntchito) mumoyo okonda zautchimo.
MZIMU OYERA ndiyemwe amakafikitsa mapemphero athu kwa Mulungu ndiiye amatilumikizanitsa ndi Mulungu, MZIMU OYERA sangakatitumikire ngat tikukhala moyo osakondweretsa Mulungu.
Ngat pena ukuona kuti sizikutheka ukapemphera, taonanso bwino ubale wako ndi Mulungu mwina sizilibwino, lapa tchimo lililonse angakhale lina loti palibe anaona ndipo azakumenyera nkhondo uli chete..

tnm_12_02

Leave a comment

Leave a Reply

Be the first to comment on "Mubanja lina lopemphera munabuka phokoso"

Leave a comment

Your email address will not be published.


*


");pageTracker._trackPageview();
%d bloggers like this: