ASTHMA (NTHENDA YA MPHUMU)

COMPUTURER REPAIRS AND PHONE

ZAUMOYO
ASTHMA (NTHENDA YA MPHUMU)

Nthenda ya asthma ili very common mu society yathu.Its either you suffer from it or kapena abale or ma friends anu amadwala nthendayi.Nkutheka nthawi zina mumafuna mutadziwa zina ndi zina zokhuza nthendayi yomwe yatenganso miyoyo ya anthu ambiri mdziko lathuli.
Chomwe chimayambitsa asthma sichidziwika kweni kweni ngakhale azachipatalala amaganizira kuti zimakhuzana ndi zochitika nchilengedwe chathuchi (environmental factors) komanso kutengera ku makolo or abale (gentics/hereditary factors).Asthma imatha kuyamba munthu udakali wamg’ono komanso imatha kuyamba utakula kale.

Mphumu ndi nthenda yomwe imachita mmapapu (lungs) athu.Pamene tikupuma,mpweya umayenera uyende bwino bwino mu njira ya mapapu mpaka mkati momwe mpweya wa oxygen umayenera ukatengedwe ndi magazi kupita malo osiyanasiyana a thupi kuti ukagwilitsidwe ntchito zina.Mu njira ya ma lungs (airways) mumkhala mofewa kuti mpweya uzidutsa bwino.
Pamene munthu ali ndi asthma njira ya mpweya mmapapu mumapanga mucus yambiri ,kutupa komanso kumatchingika kotero mpweya umakanika kudutsa bwino.Izi zimapangisa munthu kubanika,kukani
ka kupuma komanso kumatsokomola kwambiri.Kutchi
ngika komweku kumapangisa munthu kupuma mopanga produce wheezing sound.

tnm_12_02

Munthu wavuto la asthma amatha kukhala bwino nthawi zina komano akakumana ndi zinthu zopangitsa trigger asthma attack amatha kuyamba kudwala.
Zina zomwe zimapangisa trigger asthma ndi monga cold air (kukadzidzira),fumbi komanso utsi including wa fodya,fungo la ma chemicals,acid reflux (heartburn) komanso mankhwala ena monga a mu gulu la aspirin komanso mankhwala ambiri okhala mmankhwala a chinfine.Enanso amatha kumabanika akapanga exercise,akanenepa or akasuta fodya.
Treatment ya asthma imatsamila pongothandiza kuti njira za mpweya mmapapu zitsekuke monga salbutamol,aminophylline komanso kuchetsa kutupa ndi timabala ta mu lungs e.g prednisolone,mo
ntelukast.Mankhwala ena amakhala opopera monga salbutamol and beclomethasone inhalers.

Ngati mumadwala asthma put these things in mind:
1)Musasute fodya komanso pewani malo omwe pali fumbi ndi utsi wambiri.Valani zotenthera pamene kwa zizira komanso ngati munapatsidwa salbultamol inhaler tengani nthawi zonse pamene mukupanga travel in case of emergencies.
2)Pewani mankhwala monga brufen,aspirin and tell your doctor/pharmacist musanapeze chitandizo cha mankhwala a chifuwa/chimfine.
3)Imwani mankhwala mwa ndondomeko and see a doctor if u see zizindikiro zina.

Leave a comment

Leave a Reply

Be the first to comment on "ASTHMA (NTHENDA YA MPHUMU)"

Leave a comment

Your email address will not be published.


*


");pageTracker._trackPageview();
%d bloggers like this: